Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 8:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wace, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.

2. Nanyamuka mkaziyo, nacita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lace, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.

3. Ndipo pakutha pace pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kucoka m'dziko la Afilisti, naturuka kukanena za nyumba yace ndi munda wace kwa mfumu.

4. Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikuru zonse Elisa wazicita.

5. Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitisira mwana wace ananena za nyumba yace ndi munda wace kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wace Elisa anamuukitsayo?

6. Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zace zonse ndi zipatso zonse za m'munda, cicokere iye m'dziko mpaka lero lino.

7. Ndipo Elisa anafika ku Damasiko, podwala Benihadadi mfumu ya Aramu; ndipo anamuuza, kuti, Munthu wa Mulungu wadza kuno.

8. Niti mfumu kwa Hazaeli, Tenga caufulu m'dzanja lako, nukamkumike munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzacira kodi nthenda iyi?

9. Namuka Hazaeli kukakomana naye, napita naco caufulu, ndico ca zokoma zonse za m'Damasiko, zosenza ngamila makumi anai, nafika naima pamaso pace, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzacira nthenda iyi?

10. Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzacira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu.

11. Ndipo anamyang'ana cidwi, mpaka anacita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu.

12. Nati Hazaeli, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa coipa udzacitira ana a Israyeli; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.

13. Nati Hazaeli, Koma nanga kapolo wanu ali ciani, ndiye garu, kuti akacite cinthu cacikuru ici? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.

14. Ndipo anacoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wace; ameneyo ananena naye, Anakuuza ciani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzacira ndithu.

15. Ndipo kunali m'mawa mwace, anatenga cimbwi, nacibviika m'madzi, naciphimba pankhope pa mfumu, nifa; ndipo Hazaeli analowa ufumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 8