Nati Hazaeli, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa coipa udzacitira ana a Israyeli; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.