Nati Hazaeli, Koma nanga kapolo wanu ali ciani, ndiye garu, kuti akacite cinthu cacikuru ici? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.