5. Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pace pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.
6. Popeza Yehova adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magareta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikuru; nanenana wina ndi mnzace, Taonani mfumu ya Israyeli watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aaigupto, atigwere.
7. Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi aburu ao, misasa iri cimangire; nathawa, apulumutse moyo wao.
8. Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golidi ndi zobvala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa.
9. Pamenepo ananenana wina ndi mnzace, Sitirikucita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tirikukhala cete; tikacedwa kufikira kwaca, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu.