Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 6:14-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pamenepo anatumizako akavalo ndi magareta ndi khamu lalikuru, nafikako usiku, nauzinga mudziwo.

15. Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, naturuka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mudzi ndi akavalo ndi magareta. Ndi mnyamata wace ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! ticitenji?

16. Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife acuruka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.

17. Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ace kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magareta amoto akumzinga Elisa.

18. Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu ucite khungu. Ndipo iye anawakantha, nawacititsa khungu, monga mwa mau a Elisa.

19. Ndipo Elisa ananena nao, Ngati njira ndi iyi? ngati mudzi ndi uwu? munditsate ine, ndidzakufikitsani kwa munthu mumfunayo; nawatsogolera ku Samariya.

20. Ndipo kunali, pakufika ku Samariya, Elisa anati, Yehova, muwakanganulire awa maso kuti aone. Nawakanganulira Yehova maso ao, naona iwo, ndipo tapenyani, ali pakati pa Samariya.

21. Niti mfumu ya Israyeli kwa Elisa pakuwaona, Atate wanga ndiwakanthe kodi, ndiwakanthe?

22. Nati, Musawakanthe; kodi mumakantha omwe mwawagwira ndi lupanga ndi uta wanu? apatseni mkate ndi madzi adye namwe, namuke kwa mbuye wao.

23. Ndipo anwakonzera cakudya cambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzanso ku dziko la Israyeli.

24. Ndipo zitatha izi, Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lace lonse, nakwera, namangira misasa Samariya.

25. Koma m'Samariya munali njala yaikuru; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa buru unagulidwa ndalama zasiliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi ndalama zasiliva zisanu.

26. Ndipo popita mfumu ya Israyeli alikuyenda palinga, mkazi anampfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu.

27. Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? kudwale kodi, kapena popondera mphesa

28. Nanena naye mfumu, Ufunanji? Nati iye, Mnzanga uyu ananena ndi ine, Tenga mwana wako timudye lero, ndi mwana wanga timudye mawa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 6