Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 5:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo anafika kwa mfumu ya Israyeli ndi kalata, wakuti, Pakulandira kalata uyu, taonani, ndatumiza Namani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumciritse khate lace.

7. Ndipo kunali atawerenga kalatayu mfumu ya Israyeli, anang'amba zobvala zace, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumciritsa munthu khate lace? pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna cifukwa pa ine.

8. Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israyeli adang'amba zobvala zace, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zobvala zanu cifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israyeli.

9. M'mwemo: Namani anadza ndi akavalo ace ndi magareta ace, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa.

10. Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe m'Yordano kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.

11. Koma Namani adapsa mtima, nacoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kuturuka adzanditurukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wace, ndi kuweyula dzanja lace pamalopo, ndi kuciritsa wakhateyo.

12. Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m'Israyeli? ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nacoka morunda.

13. Pamenepo anyamata ace anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani cinthu cacikuru, simukadacicita kodi? koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?

14. Potero anatsika, namira m'Yordano kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wace unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 5