Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israyeli. Pamenepo anacoka, atatenga siliva: matalente khumi, ndi golidi masekeli zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi zobvala zakusintha khumi.