Koma Namani adapsa mtima, nacoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kuturuka adzanditurukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wace, ndi kuweyula dzanja lace pamalopo, ndi kuciritsa wakhateyo.