Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 5:16-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pace, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkangamiza acilandire, koma anakana.

17. Ndipo Namani anati, Mukakana, andipatse akatundu a dothi osenza nyuru ziwiri; pakuti mnyamata wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu yina, koma kwa Yehova.

18. Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ici; akalowa mbuye wanga m'nyumba ya Rimoni kulambiramo, nakatsamira pa dzanja langa, nanenso ndikagwadira m'nyumba ya Rimoni, pakugwadira ine m'nyumba ya Rimoni, Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ici.

19. Ndipo ananena naye, Pita mumtendere. Ndipo anacoka, nayenda kanthawi.

20. Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Namani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ace cimene anabwera naco; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.

21. Motero Gehazi anatsata Namani. Ndipo pamene Namani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagareta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi?

22. Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ocokera ku mapiri a Efraimu; muwapatse talente wa siliva, ndi zobvala zosintha ziwiri.

23. Nati Namani, Viole ulandire matalente awiri. Namkangamiza namanga matalente awiri a siliva m'matumba awiri, ndi zobvala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ace awiri; iwo anatsogola atazisenza.

24. Ndipo pamene anafika kumsanje anazilandira m'manjamwao, naziika m'nyumba; nauza anthuwo amuke, iwo nacoka.

25. Pamenepo analowa, na, ima kwa mbuye wace. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?

26. Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeza kodi, umo munthuyo anatembenuka pa gareta wace kukomana ndi iwe? Kodi nyengo yino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zobvala, ndi minda yaazitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo; ndi adzakazi?

27. Cifukwa cace khate la Namani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako cikhalire. Ndipo anaturuka pamaso pace wakhate wa mbu ngati cipale cofewa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 5