Ndipo Namani anati, Mukakana, andipatse akatundu a dothi osenza nyuru ziwiri; pakuti mnyamata wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu yina, koma kwa Yehova.