Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 3:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku cipululu ca Edomu.

9. Namuka mfu mu ya Israyeli, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.

10. Ndipo mfumu ya Israyeli inati, Kalanga ife! pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Moabu.

11. Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya.

12. Nati Yehosafati, Mau a Yehova ali ndi iyeyo, Pamenepo mfumu ya Israyeli, ndi Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anatsikira kuli iye.

13. Ndipo Elisa anati kwamfumuya Israyeli, Ndiri ndi ciani ndi inu? mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israyeli inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Moabu.

14. Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pace, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang'anitsani, kapena kukuonani.

15. Koma tsopano, nditengereni wanthetemya. Ndipo kunali, waothetemyayo ali ciyimbire, dzanja la Yehova linamgwera.

16. Ndipo anati, Atero Yehova, Kumbani m'cigwa muno mukhale maenje okha okha.

17. Pakuti atero Yehova, Simudzaona mphepo, kapena kuona mvula, koma cigwaco cidzadzala ndi madzi; ndipo mudzamwa inu, ndi ng'ombe zanu, ndi zoweta zanu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 3