Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 3:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israyeli m'Samariya m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.

2. Nacita coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wace ndi amace; pakuti anacotsa coimiritsa ca Baala adacipanga atate wace.

3. Koma anakangamira zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene anacimwitsa nazo Israyeli, osalekana nazo.

4. Ndipo Mesa mfumu ya Moabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israyeli ubweya wa ana a nkhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.

5. Kama kunacitika, atafa Ahabu mfumu ya Moabu anapandukana ndi mfumu ya Israyeli.

6. Ndipo mfumu Yehoramu anaturuka m'Samariya nthawi yomweyo, namemeza Aisrayeli onse.

7. Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Moabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Moabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.

8. Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku cipululu ca Edomu.

9. Namuka mfu mu ya Israyeli, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.

10. Ndipo mfumu ya Israyeli inati, Kalanga ife! pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Moabu.

11. Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 3