Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 25:18-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo mkuru wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe waciwiri, ndi olindira pakhomo atatu;

19. natenga m'mudzimo mdindo woikidwa woyang'anira ankhondo; ndi anthu asanu a iwo openya nkhope ya mfumu opezeka m'mudzimo; ndi mlembi, kazembe wa nkhondo wolembera anthu a m'dziko; ndi anthu a m'dziko makumi asanu ndi limodzi opezeka m'mudzimo.

20. Ndipo Nebuzaradani mkuru wa olindirira anawatenga, napita nao kwa mfumu ya Babulo ku Ribila.

21. Niwakantha mfumu ya Babulo, niwaphera ku Ribila m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwacotsa m'dziko lao.

22. Koma kunena za anthu otsalira m'dziko la Yuda, amene adawasiya Nebukadinezara mfumu ya Babulo, iyeyu anamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani akhale wowalamulira.

23. Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babulo adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi Yohanana mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmakati, iwo ndi anthu ao omwe.

24. Nawalumbirira Gedaliya iwo ndi anthu ao, nanena nao, Musamaopa anyamata a Akasidi; khalani m'dziko; tumikirani mfumu ya Babulo, ndipo kudzakukomerani.

25. Koma kunali mwezi wacisanu ndi ciwiri anadza Ismayeli mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yacifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Akasidi okhala naye ku Mizipa.

26. Pamenepo ananyamuka anthu onse ang'ono ndi akuru, ndi akazembe a makamu, nadza ku Aigupto; pakuti anaopa Akasidi.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 25