Koma kunali mwezi wacisanu ndi ciwiri anadza Ismayeli mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yacifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Akasidi okhala naye ku Mizipa.