Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 23:24-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi m'Yerusalemu, Yosiya anazicotsa; kuti alimbitse mau a cilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova.

25. Ndipo asanabadwe iye panalibe mfumu wolingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wace wonse, ndi moyo wace wonse, ndi mphamvu yace yonse, monga mwa cilamulo conse ca Mose; atafa iyeyu sanaukanso wina wolingana naye.

26. Koma Yehova sanakululuka mkwiyo wace waukuru waukali umene adapsa mtima nao pa Yuda, cifukwa ca zoputa zonse Manase adaputa nazo mkwiyo wace.

27. Nati Yehova, Ndidzacotsa Yudanso pamaso panga, monga umo ndinacotsera Israyeli; ndipo ndidzataya mudzi uwu ndidausankha, ndiwo Yerusalemu, ndi nyumba ndidainena, Dzina langa lidzakhala komweko.

28. Macitidwe ena tsono a Yosiya, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

29. Masiku ace Farao-Neko mfumu ya Aigupto anakwerera mfumu ya Asuri ku mtsinje wa Firate; Ddipo mfumu Yosiya anaturuka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.

30. Ndipo anyamata ace anamtengera wakufa m'gareta, nabwera naye ku Yerusalemu kucokera ku Megido, namuika m'manda ace ace. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yoahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace.Yoahazi, Yoyakimu ndi Yoyakini mafumu oipa a Yuda.

31. Yoahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu miyezi itatu m'Yerusalemu ndi dzina la mace ndiye Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina.

32. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adacita makolo ace.

33. Ndipo Faraoneko anammanga m'Ribila, m'dziko la Hamati; kuti asacite ufumu m'Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golidi.

34. Ndipo Farao-Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wace, nasanduliza dzina lace likhale Yoyakimu; koma anapita naye Yoahazi, nafika iye m'Aigupto, nafa komweko.

35. Ndipo Yoyakimu anapereka siliva ndi golidi kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m'dziko siliva ndi golidi, yense monga mwa kuyesedwa kwace, kuzipereka kwa Farao-Neko.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 23