Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 23:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo mfumu inatumiza anthu, namsonkhanitsira akulu onse a Yuda ndi a m'Yerusalemu.

2. Nikwera mfumu kumka ku nyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu pamodzi nave, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse ang'ono ndi akulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la cipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.

3. Niima mfumu paciunda, nicita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova, ndi kusunga malamulo ace, ndi mboni zace, ndi malemba ace, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a cipangano colembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.

4. Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo laciwiri, ndi olindira pakhomo, aturutse m'Kacisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi cifanizo cija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lace kumka nalo ku Beteli.

5. Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; wo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.

6. Naturutsa cifanizoco m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nacitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nacipera cikhale pfumbi, naliwaza pfumbi lace pa manda a ana a anthu.

7. Nagamula nyumba za anyamata adama okhala ku nyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsaru zolenjeka za cifanizoco.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 23