Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; wo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.