Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 2:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kabvumvulu, Eliya anacokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.

2. Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndimke ku Beteli. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Beteli.

3. Ndipo ana a aneneri okhala ku Beteli anaturukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, lode ndidziwa, khalani muli cete.

4. Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko.

5. Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli cete.

6. Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordano, Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.

7. Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordano.

8. Ndipo Eliya anagwira copfunda cace, nacipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.

9. Ndipo kunali ataoloka, Eliya anati kwa Elisa, Tapempha cimene ndikucitire ndisanacotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, Mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine.

10. Nati iye, Wapempha cinthu capatali, koma ukandipenya pamene ndicotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero at.

11. Ndipo kunacidka, akali ciyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka gareta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kabvumvulu.

12. Ndipo Elisa anapenya, napfuula, Atate wanga, atate wanga, gareta wa Israyeli ndi apakavalo ace! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zobvala zace zace, nazing'amba pakati.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 2