Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 18:12-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. cifukwa sanamvera mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira cipangano cace, ndico zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvera kapena kuzicita.

13. Caka cakhumi ndi zinai ca Hezekiya Sanakeribu mfumu ya Asuri anakwerera midzi yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.

14. Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundicokere; cimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asuri anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golidi.

15. Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca nyumba yamfumu.

16. Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golidi wa pa zitseko za Kacisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asuri.

17. Ndipo mfumu ya Asuri anatuma nduna ndi ndoda ndi kazembe ocokera ku Lakisi ndi khamu lalikuru la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima ku mcerenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku mwaniko wa otsuka nsaru.

18. Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawaturukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolemba mbiri.

19. Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri, Cikhulupiriro ici ncotani ucikhulupirira?

20. Ukuti koma ndiwo mau a pakamwa pokha, Pali uphungu ndi mphamvu ya kunkhondo. Tsono ukhulupirira yani, kuti undipandukira?

21. Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Aigupto; ndilo munthu akatsamirapo lidzamlowa m'dzanja lace ndi kulibola; atero Farao mfumu ya Aigupto kwa onse omkhulupirira iye.

22. Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamcotsera misanje yace ndi maguwa a nsembe ace, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira pa guwa la nsembe pane m'Yerusalemu?

23. Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.

24. Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata ang'ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Aigupto akupatse magareta ndi apakavalo?

25. Ngati ndakwerera malo ana wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga.

26. Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yoa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Ciaramu; popeza ticimva ici; musalankhule nafe m'Ciyuda, comveka ndi anthu okhala palinga.

27. Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 18