Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 4:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mau a Samueli anafikira kwa Aisrayeli onse. Ndipo Aisrayeli anaturuka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga m'Afeki.

2. Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisrayeli; ndipo pokomana nkhondo Aisrayeli anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.

3. Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akuru a Israyeli anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la cipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.

4. Cifukwa cace anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la cipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Pinehasi anali komweko ndi likasa la cipangano la Yehova.

5. Pakufika likasalo la cipangano la Yehova kuzithando, Aisrayeli onse anapfuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linacita cibvomezi.

6. Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kupfuula kwao, anati, Phokoso ili la kupfuula kwakukuru ku zithando za Aisrayeli litani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidzafika ku zithandozo.

7. Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! popeza kale lonse panalibe cinthu cotere.

8. Tsoka kwa ife! adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aaigupto ndi masautso onse m'cipululu ndi yomweyi.

9. Limbikani, ndipo mucite camuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Citani camuna nimuponyane nao.

10. Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisrayeli; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wace; ndipo kunali kuwapha kwakukuru; popeza anafako Aisrayeli zikwi makumi atatu a oyenda pansi.

11. Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Pinehasi, anaphedwa.

12. Ndipo munthu wa pfuko la Benjamini anathamanga kucokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zobvala zace zong'ambika, ndi dothi pamutu pace.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 4