Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akuru a Israyeli anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la cipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu.