Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 25:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira?

12. Comweco anyamata a Davide anatembenukira ku njira yao, nabwerera, nadza namuuza monga mwa mau onse awa.

13. Ndipo Davide anati kwa anthu ace, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lace. Namangirira munthu yense lupanga lace; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lace; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu.

14. Koma mnyamata wina anauza Abigayeli, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akucokera kucipululu kulankhula mbuye wathu; koma iye anawakalipira.

15. Koma anthu aja anaticitira zabwino ndithu, sanaticititsa manyazi, ndi panalibe kanthu kadatisowa, nthawi zonse tinali kuyenderana nao kubusa kuja;

16. iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo.

17. Cifukwa cace tsono mudziwe ndi kulingalira cimene mudzacita; popeza anatsimikiza mtima kucitira coipa mbuye wathu, ndi nyumba yace yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye.

18. Pomwepo Abigayeli anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoocaoca, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi ncinci za mphesa zouma zana limodzi, ndi ncinci za nkhuyu mazana awiri, naziika pa aburu.

19. Nati kwa anyamataace, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuvo mwanu. Koma sanauza mwamuna wace Nabala.

20. Ndipo kudatero pakuberekeka iye pa buru wace, natsikira pa malo obisika a m'phirilo, onani, Davide ndi anthu ace analikutsikira kwa iye; iye nakomana nao.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 25