Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 22:9-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Sauli, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Jeseyo alikufika ku Nobi, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubu.

10. Ndipo iye anamfunsira kwa Yehova, nampatsa cakudya, nampatsanso lupanga la Gotiate Mfilistiyo.

11. Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubu, ndi banja lonse la atate wace, ansembe a ku Nobi; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu.

12. Ndipo Sauli anati, Imva tsopano iwe mwana wa Ahitubu. Nayankha iye, Ndine, mbuye wanga.

13. Ndipo Sauli anati kwa iye, Munapangana dwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Jese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?

14. Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m'nyumba mwanu?

15. Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wace kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.

16. Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako.

17. Mfumu niuza asilikari akuima comzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; cifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululira. Koma anayamata a mfumu sanafuna kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova.

18. Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akubvala efodi wabafuta.

19. Ndipo anakantha Nobi ndiwo mudzi wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi aburu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.

20. Ndipo mmodzi wa ana a Ahimeleki, mwana wa Ahitubu, dzina lace ndiye Abyatara, anapulumuka, nathawira kwa Davide.

21. Ndipo Abyatara anadziwitsa Davide kuti Sauli anapha ansembe a Yehova.

22. Ndipo Davide anati kwa Abyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Sauli; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako.

23. Ukhale ndi ine, usaopa; popeza iye wakufuna moyo wanga afuna moyo wako; koma ndi ine udzakhala mosungika.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 22