Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 2:27-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziulula kwa banja la kholo lako, muja anali m'Aigupto, m'nyumba ya Farao?

28. Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israyeli, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, nabvale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israyeli?

29. Nanga umaponnderezeranji nsembe yanga ndi copereka canga, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo ucitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisrayeli, anthu anga?

30. Cifukwa cace Yehova Mulungu wa Israyeli akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Cikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.

31. Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba,

32. Ndipo udzaona masautso a mokhalamo Mulungu, m'malo mwa zabwino zonse iye akadacitira Israyeli. Banja lako lidzakhala opanda nkhalamba cikhalire.

33. Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha pa guwa langa, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako cisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri.

34. Ndipo ici cimene cidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Pinehasi, cidzakhala cizindikilo kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.

35. Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzacita monga cimene ciri mumtima mwanga ndi m'cifuniro canga; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.

36. Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi cakudya, nadzati, Mundipatsetu nchito yina ya wansembe, kuti ndikaona kakudya.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 2