Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 17:27-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamcitira munthu wakumupha iye mwakuti mwakuti.

28. Ndipo Eliabu mkuru wace anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'cipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.

29. Ndipo Davide anati, Ndacitanji tsopano? Palibe cifukwa kodi?

30. Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo.

31. Ndipo pamene mau adanena Davide anamveka, anawapitiriza kwa Sauli; ndipo iye anamuitana.

32. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Asade nkhawa munthu ali yense cifukwa ca iyeyo; ine kapolo wanu ndidzapita kuponyana ndi Mfilisti uyu.

33. Ndipo Sauli anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wace.

34. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina cimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo,

35. ndinacithamangira, ndi kucikantha, ndi kuiturutsa m'kamwa mwace; ndipo pamene cinaneliukira, ndinagwira cowa lace ndi kucikantha ndi kucipha.

36. Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi cimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 17