Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 17:17-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Jese anati kwa Davide mwana wace, Uwatengere abale ako efa watirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako;

18. nunyamule ncinci izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa cikwi cao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire cikole cao,

19. Tsono Sauli, ndi iwowa, ndi anthu onse a Israyeli, anali m'cigwa ca Ela, ku nkhondo ya Afilisti.

20. Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Jese; ndipo iye anafika ku linga la magareta, napeza khamu lirikuturuka kunka poponyanira nkhondo lirikupfuula.

21. Ndipo Israyeli ndi Afilisti anandandalitsa nkhondo zao, khamu tina kuyang'anana ndi khamu lina.

22. Ndipo Davide anasiya akatundu ace m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nalankhula abale ace.

23. Ndipo m'mene iye anali cilankhulire nao, onani cinakwerako ciwindaco, Mfilisti wa ku Gati, dzina lace ndiye Goliate, woturuka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva.

24. Ndipo Aisrayeli onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri.

25. Nati Aisrayeli, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israyeli, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi cuma cambiri, nidzampatsa mwana wace wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wace yaufulu m'Israyeli.

26. Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamcitira ciani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kucotsa tonzo lace pakati pa Israyeli? pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?

27. Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamcitira munthu wakumupha iye mwakuti mwakuti.

28. Ndipo Eliabu mkuru wace anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'cipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi.

29. Ndipo Davide anati, Ndacitanji tsopano? Palibe cifukwa kodi?

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 17