Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 15:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ace Aisrayeli; cifukwa cace tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova.

2. Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera cimene Amaleki anacitira Israyeli, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kuturuka m'Aigupto.

3. Muka tsopano, nukanthe Amaleki, nuononge konse konse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamila ndi buru.

4. Ndipo Sauli anamemeza anthu, nawawerenga ku Telayimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi.

5. Ndipo Sauli anafika ku mudzi wa Amaleki, nalalira kucigwa.

6. Ndipo Sauli anauza Akeni kuti, Mukani, cokani mutsike kuturuka pakati pa Aamaleki, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munacitira ana a Israyeli onse zabwino, pakufuma iwo ku Aigupto. Comwece Akeni anacoka pakati pa Aamaleki.

7. Ndipo Sauli anakantha Aamaleki, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri; ciri pandunji pa Aigupto.

8. Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleki, naononga konse konse anthu onse ndi lupanga lakuthwa.

9. Koma Sauli ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi ana a nkhosa, ndi zabwino zonse, sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konse konse.

10. Pamenepo mau a Yehova anafika kwa Samueli, nati,

11. Kundicititsa cisoni kuti ndinaika Sauli akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanacita malamulo anga, Ndipo Samueli anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.

12. Ndipo Samueli analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Sauli; ndipo munthu anamuuza Samueli kuti, Sauli anafika ku Karimeli, ndipo taonani, anaimika cikumbutso cace, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.

13. Ndipo Samueli anadza kwa Sauli; ndipo Sauli anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinacita lamulo la Yehova.

14. Ndipo Samueli anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndirikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndirikumva, nciani?

15. Ndipo Sauli anati, Anazitenga kwa Aamaleki; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konse konse.

16. Pomwepo Samueli ananena ndi Sauli, Imani, ndidzakudziwitsani cimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.

17. Nati Samueli, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israyeli? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israyeli,

18. Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konse konse Aamaleki akucita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 15