Ndipo Samueli analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Sauli; ndipo munthu anamuuza Samueli kuti, Sauli anafika ku Karimeli, ndipo taonani, anaimika cikumbutso cace, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.