Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 12:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo pamene munaona kuti Nahasi mfumu ya ana a Amoni inadza kuponyana nanu, munanena ndi ine, Koma mfumu itiweruze; ngakhale mfumu yanu ndiye Yehova Mulungu wanu.

13. Cifukwa cace siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu.

14. Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ace, ndi kusakana lamulo lace la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, cabwino.

15. Koma mukapanda kumvera mau a Yehova, ndi kupikisana ndi lamulo la Yehova, dzanja la Yehova lidzatsutsana nanu, monga linatsutsana ndi makolo anu.

16. Cifukwa cace tsono, imani pano, muone cinthu ici cacikuru Yehova adzacicita pamaso panu.

17. Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atomize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti coipa canu munacicita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, ncacikuru.

18. Momwemo Samueli anaitana kwa Yehova; ndipo Yehova anatumiza bingu ndi mvula tsiku lomwelo; ndipo anthu onse anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.

19. Ndipo anthu onse ananena ndi Samueli, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza coipa ici, cakuti tinadzipemphera mfumu.

20. Ndipo Samueli ananena kwa anthuwo, Musaope; munacitadi coipa ici conse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse;

21. musapambukire inu kutsata zinthu zacabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza ziri zopanda pace.

22. Pakuti Yehova sadzasiya anthu ace cifukwa ca dzina lace lalikuru; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a iye yekha.

23. Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kucimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.

24. Koma mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona, ndi mtima wanu wonse; lingalirani zinthu zazikuruzo iye anakucitirani.

25. Koma mukaumirirabe kucita coipa, mudzaonongeka, inu ndi mfumu yanu yomwe.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 12