Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 1:13-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma Hana ananena mu mtima; milomo yace inatukula, koma mau ace sanamveka; cifukwa cace Eli anamuyesa woledzera.

14. Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? cotsa vinyo wako.

15. Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndiri mkazi wa mtima wacisoni; sindinamwa vinyo kapena cakumwa cowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.

16. Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; cifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kucuruka kwa kudandaula kwanga ndi kubvutika kwanga.

17. Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israyeli akupatse copempha cako unacipempha, kwa iye.

18. Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Comweco mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yace siinakhalanso yacisoni.

19. Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wace Hana, Yehova namkumbukila iye.

20. Ndipo panali pamene nthawi yace inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna: namucha dzina lace Samueli, nati, Cifukwa ndinampempha kwa Yehova,

21. Ndipo munthuyo Elikana, ndi a pa banja lace onse, anakwera kukapereka kwa Yehova nsembe ya caka ndi caka, ndi ya cowinda cace.

22. Koma Hana sadakwera, cifukwa kuti anati kwa mwamuna wace, Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako cikhalire.

23. Ndipo Elikana mwamuna wace anati, Cita cimene cikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ace. Comweco mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wace, kufikira anamletsa kuyamwa.

24. Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye ku nyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.

25. Ndipo iwo anapha ng'ombe, nabwera naye mwanayo kwa Eli.

26. Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.

27. Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa copemphacanga ndinacipempha kwa iye;

28. cifukwa cace inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wace aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 1