Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 9:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu yina ndi kuilambira;

7. pamenepo Ine ndidzalikha Aisrayeli kuwacotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba yino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israyeli adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.

8. Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero cifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino?

9. Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adaturutsa makolo ao m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, nailambira, naitumikira; cifukwa cace Yehova anawagwetsera coipa conseci.

10. Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomo adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;

11. popeza Hiramu mfumu ya Turo adamthandiza Solomo ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golidi yemwe, monga momwe iye anafuniramo, cifukwa cace mfumu Solomo anampatsa Hiramu midzi makumi awiri m'dziko la Galileya.

12. Ndipo Hiramu anaturuka ku Turo kukaona midzi adampatsa Solomoyo, koma siinamkomera.

13. Nati, Midzi yino mwandipatsayi njotani, mbale wanga? Naicha dzina lao, Dziko lacikole, kufikira lero lino.

14. Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalenti a golidi zana limodzi mphambu makumi awiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 9