Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 9:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, atatsiriza Solomo kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi cifuniro conse ca Solomo anacikhumbaco,

2. Yehova anaonekera kwa Solomo nthawi yaciwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibeoni.

3. Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.

4. Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzicita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,

5. pamenepo Ine ndidzakhazikitsa cimpando ca ufumu wako pa Israyeli nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wacifumu wa Israyeli.

6. Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu yina ndi kuilambira;

7. pamenepo Ine ndidzalikha Aisrayeli kuwacotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba yino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israyeli adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.

8. Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero cifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino?

9. Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adaturutsa makolo ao m'dziko la Aigupto, natsata milungu yina, nailambira, naitumikira; cifukwa cace Yehova anawagwetsera coipa conseci.

10. Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomo adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;

11. popeza Hiramu mfumu ya Turo adamthandiza Solomo ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golidi yemwe, monga momwe iye anafuniramo, cifukwa cace mfumu Solomo anampatsa Hiramu midzi makumi awiri m'dziko la Galileya.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 9