Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 8:24-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. wakusungira mtumild wanu Davide atate wanga cimene mudamlonjezaco; munalankhulanso m'kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu monga lero lino.

25. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga cimene cija mudamlonjezaco, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wacifumu wa Israyeli; komatu ana ako acenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.

26. Ndipo tsopano, Mulungu wa Israyeli, atsimikizike mau anu amene munalankhula ndi mtumiki wanu Davide atate wanga.

27. Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m'Mwambamwamba zicepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.

28. Koma muceukire pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lace, Yehova Mulungu wanga, kumvera kulira ndi kupempha kwace kumene kapolo wanu apempha pamaso panu lero;

29. kuti maso anu atsegukire nyumba yino usiku ndi usana, kumalo kumene munanenako, Dzina langa lidzakhala komweko; kuti mumvere pemphero limene adzapemphera kapolo wanu lolunjika kumalo kuno.

30. Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisrayeli, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.

31. Ngati munthu akacimwira mnzace, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m'nyumba yino;

32. mverani Inu pamenepo m'mwambamo, ndipo citani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera cimo lace, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga cilungamo cace.

33. Ndipo anthu anu Aisrayeli akawakantha adani ao cifukwa ca kucimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, lodi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;

34. pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira cimo la anthu anu Aisrayeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.

35. Pamene kumwamba kwatsekeka, ndipo kulibe mvula cifukwa ca kucimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 8