Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 20:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lace lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magareta; nakamangira Samaria misasa, naponyana nao nkhondo.

2. Natumiza mithenga lrumudzi kwa Ahabu mfumu ya Israyeli, nati kwa iye,

3. Atero Benihadadi, Siliva wako ndi golidi wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga.

4. Ndipo mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndiri nazo.

5. Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golidi wako, ndi akazi ako, ndi ana ako;

6. koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m'nyumba mwako, ndi m'nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti cifuniro conse ca maso ako adzacigwira ndi manja ao, nadzacicotsa.

7. Pamenepo mfumu ya Israyeli anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti-munthu uyu akhumba coipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golidi wanga; ndipo sindinamkaniza.

8. Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musabvomereze.

9. Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba kundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzacita, koma ici sindingacicite. Nicoka mithengayo, nimbwezera mau.

10. Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati pfumbi la Samaria lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.

11. Ndipo mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakubvulayo.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 20