Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 2:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Cita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wace waimvi utsikire kumanda ndi mtendere.

7. Koma ucitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Gileadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.

8. Ndipo taona uli naye Simeyi mwana wa Gera wa pfuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikuru tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordano, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga,

9. Ndipo tsono, usamuyesera iye wosacimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumcitira iye, nutsitsire mutu wace waimvi ndi mwazi kumanda.

10. Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide.

11. Ndipo masiku ace akukhala Davide mfumu ya Israyeli anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu citatu anakhala mfumu ku Yerusalemu.

12. Tsono Solomo anakhala pa mpando wacifumu wa Davide atate wace, ndipo ufumu wace unakhazikika kwakukuru.

13. Pomwepo Adoniya mwana wa Hagati anadza kwa Batiseba amai wace wa Solomo, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene.

14. Anatinso, Ndiri nanu mau, Nati iye, Tanena.

15. Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisrayeli onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Mulungu.

16. Ndipo tsopano, ndikupemphani pempho limodzi, musandikaniza. Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Tanena.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 2