Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 19:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Citaleka cibvomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo, Utaleka mota panali bata la kamphepo kayaziyazi.

13. Ndipo atamva Eliya, anapfunda nkhope yace ndi copfunda cace, naturuka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Ucitanji kuno, Eliya?

14. Nati iye, Ndacitira cangu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israyeli ataya cipangano canu, nagumula maguwa a nsembe anu, napha aneneri anu ndi lupanga; ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuucotsa.

15. Ndipo Yehova anati kwa iye, Bwerera ulendo wako, udzere kucipululu kumka ku Damasiko, ndipo utafikako udzoze Hazaeli akhale mfumu ya Aramu;

16. ukadzozenso Yehu mwana wa Nimsi akhale mfumu ya Israyeli; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abelimehola akhale mneneri m'malo mwako.

17. Ndipo kudzacitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaeli; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu,

18. Ndiponso ndidasiya m'lsrayeli anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala maondo ao, osampso-mpsona ndi milomo yao.

19. Tsono anacokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa cikhasu ng'ombe ziwiri ziwiri magori khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa gori lakhumi ndi ciwiri; ndipo Eliya anamka kunali iyeyo, naponya copfunda cace pa iye.

20. Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndithange ndakapsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera, ndakucitanji?

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 19