Tsono anacokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa cikhasu ng'ombe ziwiri ziwiri magori khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa gori lakhumi ndi ciwiri; ndipo Eliya anamka kunali iyeyo, naponya copfunda cace pa iye.