Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 16:20-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Macitidwe ena tsono a Zimri, ndi ciwembu anacicitaco, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

21. Pamenepo anthu a Israyeli anagawika pakati, anthu ena anatsata Tibini mwana wa Ginati kumlonga ufumu, ena natsata Omri.

22. Koma anthu akutsata Omri anapambana iwo akutsata Tibini mwana wa Ginati; nafa Tibini, Omri nakhala mfumu.

23. Caka ca makumi atatu ndi cimodzi ca Asa mfumu ya Yuda, Omri anayamba kukhala mfumu ya Israyeli, nakhala zaka khumi ndi ziwiri; ku Tiriza anali mfumu zaka zisanu ndi cimodzi.

24. Ndipo anagula kwa Semeri citunda ca Samaria ndi matalente awiri a siliva, namanga pacitundapo, nacha dzina lace la mudzi anaumanga Samaria, monga mwa dzina la Semeri mwini citundaco.

25. Koma Omri anacimwa pamaso pa Yehova, nacita zoipa koposa onse adamtsogolerawo.

26. Nayenda m'njira yonse ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi chimo lace anacimwitsa nalo Aisrayeli, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli ndi zacabe zao.

27. Ndipo macitidwe ena a Omri anawacita, ndi mphamvu yace anaionetsa, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

28. Nagona Omri ndi makolo ace, naikidwa m'Samaria; ndipo Ahabu mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.

29. Ndipo caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omri analowa ufumu wa Israyeli, nakhala Ahabu mwana wa Omri mfumu ya Israyeli m'Samaria zaka makumi awiri mphambu ziwiri.

30. Ndipo Ahabu mwana wa Omri anacimwa pamaso pa Yehova koposa onse adamtsogolerawo.

31. Ndipo kunali monga ngati kunamcepera kuyenda m'macimo a Yerobiamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebeli mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Azidoni, natumikira Baala, namgwadira,

32. Nammangira Baala guwa la nsembe m'nyumba ya Baala anaimanga m'Samaria.

33. Ahabu anapanganso cifanizo; ndipo Ahabu amene anapambana mafumu onse a Israyeli adamtsogolerawo, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli,

34. M'masiku ace Hiyeli wa ku Beteli anamanga Yeriko; pokhazika maziko ace anadzifetsera Abiramu mwana wace woyamba, poimika zitseko zace anadzifetsera Zegubi mwana wace wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 16