Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 16:14-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Tsono macitidwe ena a Ela, ndi nchito zace zonse, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

15. Ndipo caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Asa mfumu ya Yuda, Zimri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti.

16. Koma anthu aja omangira misasa anamva kuti Zimri wacita ciwembu, nakanthanso mfumu; cifukwa cace tsiku lomwelo Aisrayeli onse a kumisasa anamlonga Omri kazembe wa nkhondo akhale mfumu ya Israyeli.

17. Ndipo Omri anacoka ku Gibetoni, ndi Aisrayeli onse naye, nakamangira misasa Tiriza.

18. Kunali tsono, pakuona Zimri kuti nkhondo yalowa m'mudzi, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi mota nyumba ya mfumu, nafa;

19. cifukwa ca macimo ace anacimwawo, pakucita coipa pamaso pa Yehova; popeza anayenda m'njira ya Yerobiamu, ndi m'chimo lace anacimwa nalolo, nacimwitsa nalo Aisrayeli.

20. Macitidwe ena tsono a Zimri, ndi ciwembu anacicitaco, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

21. Pamenepo anthu a Israyeli anagawika pakati, anthu ena anatsata Tibini mwana wa Ginati kumlonga ufumu, ena natsata Omri.

22. Koma anthu akutsata Omri anapambana iwo akutsata Tibini mwana wa Ginati; nafa Tibini, Omri nakhala mfumu.

23. Caka ca makumi atatu ndi cimodzi ca Asa mfumu ya Yuda, Omri anayamba kukhala mfumu ya Israyeli, nakhala zaka khumi ndi ziwiri; ku Tiriza anali mfumu zaka zisanu ndi cimodzi.

24. Ndipo anagula kwa Semeri citunda ca Samaria ndi matalente awiri a siliva, namanga pacitundapo, nacha dzina lace la mudzi anaumanga Samaria, monga mwa dzina la Semeri mwini citundaco.

25. Koma Omri anacimwa pamaso pa Yehova, nacita zoipa koposa onse adamtsogolerawo.

26. Nayenda m'njira yonse ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi chimo lace anacimwitsa nalo Aisrayeli, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli ndi zacabe zao.

27. Ndipo macitidwe ena a Omri anawacita, ndi mphamvu yace anaionetsa, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

28. Nagona Omri ndi makolo ace, naikidwa m'Samaria; ndipo Ahabu mwana wace analowa ufumu m'malo mwace.

29. Ndipo caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omri analowa ufumu wa Israyeli, nakhala Ahabu mwana wa Omri mfumu ya Israyeli m'Samaria zaka makumi awiri mphambu ziwiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 16