Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 12:17-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Kama ana aja a Israyeli akukhala m'midzi ya Yuda, Rehabiamu anakhalabe mfumu yao.

18. Pamenepo mfumu Rehabiamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisrayeli onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehabiamu anafulumira kulowa m'gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.

19. Motero Aisrayeli anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.

20. Ndipo kunali, atamva Aisrayeli onse kuti Yerobiamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisrayeli onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma pfuko lokha la Yuda.

21. Ndipo Rehabiamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi pfuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israyeli, kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu mwana wa Solomo.

22. Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati,

23. Lankhula kwa Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti,

24. Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israyeli, bwererani yense kunyumba kwace; popeza cinthuci cacokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.

25. Ndipo Yerobiamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efraimu, nakhalamo, naturukamo, namanga Penueli.

26. Ndipo Yerobiamu ananena m'mtima mwace, Ufumuwu udzabwereranso ku nyumba ya Davide.

27. Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda.

28. Potero mfumu inakhala upo, napanga ana a ng'ombe awiri agolidi, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisrayeli inu milungu yanu imene inakuturutsani m'dziko la Aigupto.

29. Ndipo anaimika mmodzi ku Beteli, naimika wina ku Dani.

30. Koma cinthu ici cinasanduka: chimo, ndipo anthu anamka ku mmodziyo wa ku Dani.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 12