Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 12:16-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu siinawamvera iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu Aisrayeli inu; yang'aniranitu, nyumba yako, Davide. Momwemo Aisrayeli anacoka kumka ku mahema ao.

17. Kama ana aja a Israyeli akukhala m'midzi ya Yuda, Rehabiamu anakhalabe mfumu yao.

18. Pamenepo mfumu Rehabiamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisrayeli onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehabiamu anafulumira kulowa m'gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.

19. Motero Aisrayeli anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.

20. Ndipo kunali, atamva Aisrayeli onse kuti Yerobiamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisrayeli onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma pfuko lokha la Yuda.

21. Ndipo Rehabiamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi pfuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israyeli, kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu mwana wa Solomo.

22. Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati,

23. Lankhula kwa Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti,

24. Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israyeli, bwererani yense kunyumba kwace; popeza cinthuci cacokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.

25. Ndipo Yerobiamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efraimu, nakhalamo, naturukamo, namanga Penueli.

26. Ndipo Yerobiamu ananena m'mtima mwace, Ufumuwu udzabwereranso ku nyumba ya Davide.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 12