Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 10:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Tsono kulemera kwace kwa golidi anafika kwa Solomo caka cimodzi kunali matalenti mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi liimodzi a golidi,

15. osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabu, ndi wa akazembe onse a madera.

16. Ndipo mfumu Solomo anapanga zikopa mazana awiri zagolidi wonsansantha, cikopa cimodzi cinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi.

17. Ndi malihawo mazana atatu a golidi wonsansantha, libawo limodzi linapangidwa ndi miyeso itatu ya golidi; ndipo mfumu inazisungira zonse m'nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano.

18. Ndipo mfumu inapanga mpando waukulu wacifumu waminyanga, naukuta ndi golidi woyengetsa.

19. Mpandowo wacifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wacifumu panali pozungulira kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo.

20. Ndipo anaimikamikango khumi ndi iwiri mbali yina ndi yina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko liri lonse tina simunapangidwa wotere.

21. Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomo zinali zagolidi, ndi zotengera zonse za nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano zinali zagolidi yekha yekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva ana ngoyesedwa opanda pace masiku onse a Solomo.

22. Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisi zinafika, kamodzi zitapita zaka zitatu, ziri nazo golidi, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za maanga maanga.

23. Ndipo mfumu Solomo anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa cuma ndi nzeru.

24. Ndipo anthu onse a pa dziko anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zace zimene Mulungu analonga m'mtima mwace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 10