Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 1:17-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu.

18. Ndipo tsopano taonani, Adoniva walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa.

19. Ndipo iye anapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi Abyatara wansembe, ndi Yoabu kazembe wa nkhondo; koma Solomo mnyamata wanu sanamuitana.

20. Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisrayeli onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye,

21. Mukapanda kutero, kudzacitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ace, ine ndi mwana wanga Solomo tidzayesedwa ocimwa.

22. Ndipo taona, iye ali cilankhulire ndi mfumu, Natani mneneriyo analowamo.

23. Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yace pansi pamaso pa mfumu.

24. Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wacifumu?

25. Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pace, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.

26. Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomo mnyamata wanu, sanatiitana.

27. Cinthu ici cacitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitsa mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wacifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye?

28. Tsono mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Batiseba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu.

29. Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m'nsautso monse,

30. zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Zoonadi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 1