Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yohane 21:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa akuphunzira ace ku nyanja ya Tiberiya. Koma anadzionetsera cotere.

2. Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wochedwa Didimo, ndi Natanayeli wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedayo, ndi awiri ena a akuphunzira ace.

3. Simoni Petro ananena nao, ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anaturuka, nalowa m'ngalawa; ndipo m'usiku muja sanagwira kanthu.

4. Koma pakuyamba kuca, Yesu anaimirira pam bali pa nyanja, komatu akuphunzirawo sanadziwa kuti ndiye Yesu.

5. Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha iye, lai.

6. Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka ku mbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza, Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka cifukwa ca kucuruka nsomba.

7. Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadzibveka maraya a pathupi, pakuti anali wamarisece, nadziponya yekha m'nyanja.

8. Koma akuphunzira ena anadza m'kangalawa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo.

9. Ndipo pamene anaturukira pamtunda, anapenya moto wamakara pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate.

10. Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano,

11. Cifukwa cace Simoni Petro anakwera m'ngalawa nakokera khoka kumtunda Iodzala ndi nsomba zazikuru, zana limodzi, ndi makumiasanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinacuruka kotere, kokha silinang'ambika.

Werengani mutu wathunthu Yohane 21