Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 17:3-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.

4. Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akuru osati owerengeka.

5. Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa acabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nacititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira ku nyumba ya Yasoni, nafuna kuwaturutsira kwa anthu.

6. Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akuru a mudzi, napfuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso;

7. amene Yasoni walandira; ndipo onsewo acita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu yina, Yesu.

8. Ndipo anabvuta anthu, ndi akuru a mudzi, pamene anamva zimenezi.

9. Ndipo pamene analandira cikole kwa Yasoni ndi enawo, anawamasula.

10. Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Sila usiku kunka ku Bereya; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda.

11. Amenewa anali mfulu koposa a m'Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.

12. Ndipo ambiri a iwo anakhulupira; ndi akazi a Cihelene omveka, ndi amuna, osati owerengeka.

13. Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereyanso, anadza komwekonso, nautsa, nabvuta makamu.

14. Pomwepo abale anaturutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Sila ndi Timoteo anakhalabe komweko.

15. Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Sila ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi cangu conse, anacoka.

16. Pamene Paulo analindira iwo pa Atene, anabvutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano.

17. Cotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.

18. Ndipo akukonda nzeru ena a Epikureya ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, ici ciani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zacilendo, cifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.

19. Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa ciphunzitso ici catsopano ucinena iwe?

20. Pakuti ufika nazo ku makutu athu zacilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani?

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 17