Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 8:22-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo panali limodzi la masiku aja, iye analowa m'ngalawa, ndi ophunzira ace; nati kwa iwo, Tiolokere ku tsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.

23. Ndipo m'mene iwo anali kupita pamadzi, iye anagona tulo, Ndipo panyanja panatsikira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, analimkuopsedwa.

24. Ndipo anadza kwa iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika, Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ace a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa batao

25. Ndipo iye anati kwa iwo, Cikhulupiriro canu ciri kuti? Ndipo m'kucita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera iye?

26. Ndipo iwo anakoceza kudooko ku dziko la Agerasa, ndilo Iopenyana ndi Galileya.

27. Ndipo ataturuka pamtanda iye, anakomana naye mwamuna wa kumudzi, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanabvala cobvala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda.

28. Ndipo pakuona Yesu, iye anapfuula, nagwa pansi pamaso pace, nati ndi mau akuru, Ndiri naco ciani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikupemphani Inu musandizunze.

Werengani mutu wathunthu Luka 8