Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 5:30-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ace nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ocimwa?

31. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing'anga; koma akudwala ndiwo.

32. Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ocimwa kuti atembenuke mtima,

33. Ndipo iwo anati kwa iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawiri kawiri, ndi kucita mapemphero; cimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.

34. Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?

35. Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.

36. Ndipo iye ananenanso fanizo kwa iwo, kuti, Palibe munthu ang'amba cigamba ca maraya arsopano, naciphatika pa maraya akale; cifukwa ngati atero, angong'ambitsa atsopanowo, ndi cigamba ca atsopanowo sicidzayenerana ndi akalewo.

37. Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m'matumba akale; cifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.

38. Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m'matumba atsopano.

39. Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma.

Werengani mutu wathunthu Luka 5