Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 16:13-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.

14. Koma Marisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka.

15. Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; cifukwa ici cimene cikuzika mwa anthu ciri conyansa pamaso pa Mulungu.

16. Cilamulo ndi aneneci analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu ali yense akangamira kulowamo.

17. Kuti kumwamba ndi dziko lapansi zicoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono ka cilamulo kagwe nkwapatali.

18. Yense wakusudzula mkazi wace, nakwatira wina, acita cigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, acita cigololo,

19. Ndipo panali munthu mwini cuma amabvala cibakuwa ndi nsaru yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;

20. ndipo wopemphapempha wina, dzina lace Lazaro, adaikidwa pakhomo pace wodzala ndi zironda,

21. ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini cumayo; komatu agarunso anadza nanyambita zirondazace.

22. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka ku cifuwa ca Abrahamu; ndipo mwini cumayo adafanso, naikidwa m'manda.

23. Ndipo m'Hade anakweza maso ace, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'cifuwa mwace.

24. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundicitire cifundo, mutome Lazaro, kuti abviike nsonga ya cala cace m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto.

25. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukila kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.

26. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikuru, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kucokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kucokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso.

27. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume ku nyumba ya atate wanga;

28. pakuti ndirinao abale asanu; awacitire umboni iwo kuti iwonso angadze ku malo ana a mazunzo.

29. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo.

30. Koma anati, lai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wocokera kwa akufa adzasandulika mtima.

Werengani mutu wathunthu Luka 16