Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 21:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma amantha, ndi osakhulupira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi acigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, colandira cao cidzakhala m'nyanja yotentha ndi mota ndi sulfure; ndiyo imfa yaciwiri.

9. Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu Ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.

10. Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka ku phiri lalikuru ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika m'Mwamba kucokera kwa Mulungu,

11. ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwace kunafanana ndi mwala wa mtengo wace woposa, Dgati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;

12. nukhala nalo linga lalikuru ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi mama olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israyeli;

13. kum'mawa zipata zitatu, ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwela zipata zitatu, ndi kumadzulo zipata zitatu.

14. Ndipo linga la mudzi linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 21