Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Cibvumbulutso 21:12-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. nukhala nalo linga lalikuru ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi mama olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israyeli;

13. kum'mawa zipata zitatu, ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwela zipata zitatu, ndi kumadzulo zipata zitatu.

14. Ndipo linga la mudzi linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa.

15. Ndipo iye wakulankhula ridi ine anali nao muyeso, bango lagolidi, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zace, ndi linga lace.

16. Ndipo mzinda ukhala wampwamphwa; utali wace ulingana ndi kupingasa kwace: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wace, ndi kupingasa kwace, ndi kutalika kwace zilingana.

17. Ndipo anayesa linga lace, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo.

18. Ndipo mirimo ya linga lace ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwagolidi woyengeka, wofanana ndi mandala oyera.

19. Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundu mitundu; mazikooyamba, ndi yaspi; aciwiri, ndi safiro; acitatu, ndi kalikedo; acinai, ndi smaragido;

20. acisanu, ndi sardoau; acisanu ndi cimodzi, ndi sardiyo; acisanu ndi ciwiri, ndi krusolito; acisanu ndi citatu, ndi berulo; acisanu ndi cinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndt cimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi ciwiri, ndi ametusto.

21. Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; citseko ciri conse pa cokha ca ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda ma golidi woyengeka, ngati mandala openyekera.

22. Ndipo siridinaona Kacisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kacisi wace.

23. Ndipo 1 pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yace ndiye Mwanawankhosa.

24. Ndipo 2 amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwace; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.

25. Ndipo 3 pa zipata zace sipatsekedwa konse usana, 4 (pakuti sikudzakhala usiku komweko);

26. ndipo 5 adzatenga ulemerero ndi ulemu wa amitundu nadzalowa nao momwemo;

27. ndipo 6 simudzalowa konse momwemo kanthu kali konse kosapatulidwa kapena iye wakucita conyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa 7 m'buku la moyo la Mwanawankhosa.

Werengani mutu wathunthu Cibvumbulutso 21